Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 230
Miyambi ya Patsokwe
ungadzazifune.
Ukakhuta umawotcha nkhokwe.
-Tisamapondereze ena powachotsera mwayi wopeza zosowa
zawo. Ukakhala pabwino usamataye zinthu chifukwa njala ikho-
za kukupwetekanso.
Ukakhuta usamatsinkhire anzako ndiwo.
-Si bwino kupondereza ena ife tikakhala pabwino.
Ukakhuta usamatukwane yemwe wakupatsa chakudya.
-Munthu akakhuta amaganiza kuti njala singamupwetekenso.
Choncho amayamba kunyoza komanso kuchitira mwano amene
amamuthandiza. Tisamachite khalidwe limeneli.
Ukakoka dzungu, umakoka ndi ana ake omwe.
-Munthu ukakwatira kapena kukwatiwa, osasakonda munthu
yekhayo komanso abale ake.
Ukakoka khoka, umakokanso zonse zomwe zilimo.
-Munthu ukakwatira kapena kukwatiwa osasakonda munthu
yekhayo komanso abale ake.
Ukakongola kwatiwa, chifukwa kunyansa kumachita
kubwera.
-Mwayi ukapezeka tiziugwiritsa ntchito.
Ukakongola leka thyonyo.
-Ukakhala wokongola usamanyoze anzako chifukwa za mawa
sizidziwika, mwina ukhoza kudzakhala ndi chilema m’tsogolo.
Ukakwatirana ndi nyani chifukwa cha chuma chake, chu-
macho chimatha, iwe umatsala ndi nyaniyo.
-Ndi bwino kumayang’ana munthu wakhalidwe labwino
ukamafuna kukwatira m’malo motsatira chuma chomwe ndi
mchira wakhoswe.
229