Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 23
Miyambi ya Patsokwe
Chaipira Galu kuluma Mbuzi.
-Munthu anganene mawuwa akamadandaula ndi mavuto omwe
amulepheretsa kuchita zinthu zimene amafuna. Munthu an-
ganenenso mawuwa podandaula zinthu zopanda chilungamo
zimene ena amuchitira.
Chakanachakana, dazi lilibe mankhwala.
-Pali zinthu zina zomwe ndi umunthu wathu sitingazithe. Zote-
rezi tiyenera kuvomereza kuti zikhale mmene zilili ndi kukhuti-
ra ndi zimene tili nazo.
Chakanachakana, Kalulu sasenda nguwo.
-Tizivomereza ngati zinthu zavuta, osamachita ukamberembere.
Chako n’chako sichilingana n’chamwini.
-Chinthu chako umachigwiritsa ntchito mwanjira iliyonse, koma
chamwini umachiopa.
Chakomera Mbuzi kugunda Galu, Galu akati agundeko akuti
wapenga.
-Osamachita zinthu mokondera kapena kumachitira ena
nkhanza tikudziwa kuti ena atiikira kumbuyo.
Chakomera Mbuzi kugunda Galu, Galu akati alumeko akuti
waboola nguwo.
-Osamachita zinthu mokondera kapena kumachitira ena
nkhanza tikudziwa kuti ena atiikira kumbuyo.
Chakomera nzako umasimba.
-Ndi bwino kumayamikirako zabwino zimene ena achita.
Chakometsa Ntchentche, inachilimika kuuluka.
-Kuti munthu upeze bwino umafunika kukhala ndi podalira ko-
manso kuchita khama.
Chakonda mnzako mlekere, mawa chidzakonda iwe.
-Mnzathu akachita mwayi si bwino kumuchitira nsanje
22