Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 227
Miyambi ya Patsokwe
Uhule ndi mtima.
-Munthu sakhala hule chifukwa cha mmene akuonekera koma
mtima wake.
Ukabwereka miyendo ya munthu, umapita kulikonse kumene
iyeyo akufuna.
-Munthu amene ali ndi ngongole sakhala ndi ufulu wochita
zimene akufuna ndi ndalama yake.
Ukachedwa umagula khutu.
-Mwambiwu umachenjeza munthu amene amachita zinthu
mochedwa kapena mwachidodo. M’malo mogula nyama
yabwino amakapena kuti latsala ndi khutu.
Ukachenjera sunona.
-Nthawi zambiri amene amakonda kuyankhulayankhula kapena
ochenjeretsa amakhala opanda nzeru. Chimodzimodzinso okon-
gola, amangokongola nkhope koma n’kukhala opanda nzeru
kapena opanda khalidwe.
Ukachoka usamachitire dziko chipongwe, umakumbukira
pokabwera.
-Pochoka pamalo umayenera kuchoka mwaulemu kuti mawa
adzakulandirenso.
Ukachoka usamatseke potulukira ndi mwala koma mayani.
-Osamachoka pankhomo utawonongapo chifukwa tsiku lina
udzabwerera.
Ukadya, umadziwa azungu ndi alendo.
-Ukalemera usamanyoze anzako chifukwa ntchito ikatha, sudza-
khalanso ndi azungu koma abale ako. Komanso anzako omwe
unkawanyoza. Pang’ono mwambiwu umalimbikitsa tsankho.
Mukadzaugwiritsa ntchito musadzadabwe apolisi akadza-
kumangani.
226