Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 226

Miyambi ya Patsokwe Udakula bwanji wopanda tsinde? -Tisamaiwale abale komanso anthu ena omwe atithandiza kuti tifike pamene tili lero. Udam’dyeranji pholokoto anzako akudya kawerawera? -Tizigwira ntchito molimbika kuti tipeze zosowa zathu. Polima timawerama osati kuimirira. Udaotha chichiri cha ukonde. -Chichiri chimathandiza kuti ukonde ukhale wokungika. Mawu- wa amagwiritsidwa ntchito potanthauza munthu yemwe wapal- amula kapena kulakwira anthu omuthandiza. Ufiti ndi mawu. -Tisamayankhule zonyoza kapena kutukwana chifukwa china chikachitika anthu amaloza ife. Ufulu umabweza ufulu. -Ukachitira anzako zabwino nawonso amakuchitira zabwino. Ufulu wa ng’ombe wogwedeza mchira. -Pali anthu ena omwe amati munthu akawachitira zabwino sathokoza. Monga mmene ng’ombe imachitira akaipatsa chakudya, chinthu chimene imachita ikamayamikira ndi kugwedeza mchira, sibweza kalikonse. Ufumu wanji wa Kadzidzi wokhala pachitsa? -Mfumu isamangokhala neng’a, koma izichita zinthu zomwe zingathandize anthu ake. Ufune kaya uleke, kulidetsa tsitsi ndi ufulu. -Chilichonse chili ndi nthawi. Ufunthafuntha mphuku, mbiri nja khoswe. -Munthu akakhala woipa kapena wochenjeretsa amasowa mtendere, chifukwa chilichonse choipa amangoti wachita ndiwe. 225