Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 225
Miyambi ya Patsokwe
Ubale waufulu uli pamalemba.
-Anthu amagwirizana akakhala patali, koma akakhala pamodzi
sachedwa kukhulana.
Ubwenzi wa “ponda apo mpondepo.”
-Chimenechi ndi chikondi chenicheni chochitira zinthu limodzi.
Ubwenzi wa galu uli kumchira.
-Ubwenzi weniweni uyenera kumakhala ndi ntchito zake, osati
kumangonena pakamwa pokha kuti awa ndi anzanga, zika-
wavuta n’kuwathawa.
Ubwenzi wa madzi ndi nsomba.
-Ubwenzi weniweni umakhalapo ngati anthu amakhalira
limodzi osasiyana zivute zitani.
Ubwenzi wa Nkhwazi woyanjana polira.
-Polira pokha ndi pamene Nkhwazi zimagwirizana. Koma ikag-
wira nsomba imadya yokha. Mawu amenewa amanena za mun-
thu amene amakhala mnzako akavutika, koma zikamamuyen-
dera saoneka. Ubwenzi weniweni umaoneka zinthu zikavuta.
Ubwenzi wa nsomba wosalekana ndi madzi.
-Ubwenzi wa nsomba ndi madzi ndi weniweni. Pamene madzi
aphwera nsomba imafa. Mawuwa amatanthauza ubwenzi weni-
weni woferana.
Ubwino wa dzuwa umaoneka likapita.
-Munthu wabwino amadziwika akapita. Mwachitsanzo, ena
amazindikira kuti mkazi kapena mwamuna wawo anali
wabwino banja likatha. Nthawi zambiri amazindikira zimenezi
akakwatirana ndi chilombo.
Uchembere n’kudyerana.
-Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi bwino kumuchitira
zabwino.
224