Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 224

Miyambi ya Patsokwe zikuluzikulu zimatheka pozichita pang’onopang’ono komanso ngati titapirira. Tulo n’timodzi, usiyana ndi mkonono. -Tonse ndi anthu koma timasiyana khalidwe. Tulo ndi imfa, susankha pogonera. -Zinthu zina zimafika mosayembekezera monga imfa. Tulo ndi nkhondo, timagonetsa anamalira. -Tizichita zinthu mwamphamvu komanso molimba mtima ngati mmene tulo timachitira. 223