Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 223
Miyambi ya Patsokwe
Tsoka lilibe fungo.
-Tsoka limabwera mwadzidzidzi.
Tsoka limayambira kumwendo.
-Tsoka limayamba pang’onopang’ono. Anthu ena a ku Africa
kuno amakhulupirira kuti munthu akamayenda ndiyeno n’ku-
puntha, ndiye kuti kumene akupitako akapezako matenda
kapena maliro. Mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena kuti
uli ndi tsoka lalikulu. Tsoka limayambira pa kanthu kakang’ono
komwe anthu sangakaganizire kuti kangayambitse vuto laliku-
lu.
Tsoka msinde chimanga chilinda moto.
-Mawuwa amatanthauza kuchita tsoka lalikulu.
Tsoka n’kusuzumira m’chizombwe.
-Munthu wachidwi kwambiri amatha kukumana ndi mavuto.
Mwachitsanzo, posuzumira pachulu amatha kulavuliridwa ndi
njoka.
Tsoka ndi mphwayi, ukafuna kanthu koma kuyesa.
-Munthu wamphwayi sangapeze zimene akufuna. Tizichita kha-
ma tikamachita zinthu.
Tsoka sasimba, koma mwayi.
-Ukapulumuka tsoka, si bwino kukakamira khalidwe lomwe
lakubweretsera tsokalo chifukwa mwina pambuyo pake ukhoza
kutaya moyo wako kapena osapulumukanso.
Tsoka silinunkha.
-Tsoka limabwera mwadzidzidzi.
Tsokonombwe adatha mtunda n’kudumpha.
-Nthawi zina ndi bwino kuchita zinthu mosathamanga komanso
ndi bwino kulimbikira kuti zomwe ukufuna zitheke. Zinthu
222