Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 222
Miyambi ya Patsokwe
Tsoka la mnzako likupatse nzeru.
-Wina akalakwitsa chinachake, ndi bwino kumaphunzirapo kan-
thu kuti tisabwerezenso zomwezo. Moyo ndi waufupi kwambiri
kuti munthu aphunzire pa zolakwa zake zokha.
Tsoka la mnzako n’lakonso.
-Nthawi zina tsoka la ena limakhudzanso anthu ena, monga
oyandikana nawo nyumba. Tizithandiza ena akakhala
m’mavuto.
Tsoka la msinde, chimanga chilinda moto.
-Misinde imacha mwamsanga moti anthu amayamba kuidya
chimanga chisanakhwime. Anthu ena amazunza anzawo mosa-
samala kanthu kuti ndi abale awo.
Tsoka la Nkhuku lopita kumanda nthenga zokha.
-Limeneli ndi tsoka lalikulu kwambiri lomwe munthu anga-
kumane nalo. Nkhuku ikafa maliro ake saikidwa m’manda. Ku-
manda kumangopita nthenga zokha basi.
Tsoka la mfutso lobwerera pamoto kawiri.
-Limeneli ndi tsoka lalikulu kwambiri lomwe munthu anga-
kumane nalo.
Tsoka likakuda Kamba amaoneka ngati mwala.
-Kamba ngati sakusuntha amaoneka ngati mwala. Nkhani zina
zimakhala zosamvetsetseka. Wina akhoza kudwala mwakayaka-
ya koma wina wolimba n’kumwalira kusiya wodwalayo.
Tsoka likalimba amakuluma ndi galu wako yemwe.
-Zinthu zikati zivute, nthawi zina anthu amene umawadalira ndi
amene amakutaya.
Tsoka likalimba umakuotcha ndi mkute.
-Zinthu zikati zivute, nthawi zina anthu amene umawadalira ndi
amene amakutaya.
221