Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 221
Miyambi ya Patsokwe
Tsatanetsatane ndi njira.
-Munthu poyankhula sangathe kunena ndendende zonse
zimene waona kapena zimene wina wanena.
Tulo ndi nkhondo, tinagonetsa anamalira.
-Ena amaganiza kuti, kuti asonyeze kuti amakonda kwambiri
m’bale wawo amene wamwalira, afunika kulira usiku onse. Ko-
ma tulo tilibe masewera, timatha kugonetsa munthu wotereyu.
Tsekera lili pachipadzo.
-Udzu wabwino umasadzulidwa ndi nsungwi.
Chimodzimodzinso mwana, kuti akule bwino timayenera
kuyambiratu kusadza makhalidwe ake oipa adakali wamng’ono.
Tsiku limodzi silivunda nyama.
-Zinthu zina sizingatheke tsiku limodzi, pamafunika nthawi.
Tsiku limodzi siliwoza mbewa.
-Nthawi zina ndi bwino kudikira pochita zinthu chifukwa
tikachita mofulumira nthawi zina zinthuzo sizichitika bwino.
Zinthu zina sizingatheke tsiku limodzi, pamafunika nthawi.
Tsiku lofera nyani mitengo yonse imaterera.
-Anyani ena ankadalira mitengo kuti agalu akamabwera an-
gokwerapo. Koma tsiku lina agalu akubwera anyaniwo anapeza
kuti mitengo yonse inali yoterera moti anagwidwa. Tizikonze-
kera zinthu zomwe zikhoza kutigwera.
Tsitsi likakula udzasowa wokumeta.
-Munthu wosamva amamva akakumana ndi mavuto.
Tsoka chitambe.
-Chitambe chimakhwima nsanga kuposa masamba ena. Zimene-
zi zimachititsa kuti chikhale choyambirira kudyedwa. Mwana
woyamba ndi amene amakumana ndi zoopsa. Tisamathamangi-
re kuchita zinthu tisanaganize bwino.
220