Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 220

Miyambi ya Patsokwe cha paulendo chifukwa sitikudziwa zimene zingatichitikire. Tokoma sitichedwa kutha, ndaonera dowe. -Zinthu zabwino sizichedwa kutha. Tisamaike mtima wathu pa zinthu zosakhalitsa. Tokoma sitikuti “leke.” -Zabwino sizingauze munthu kuti asiye, umafunika wekha kud- ziwa kuti pamene ndafikapa ndakwana. Tokoma sitioneka tsiku limodzi. -Tizifatsa ndi kumaupeza mtima chifukwa zabwino zimabwera pang’onopang’ono. Tokoma tidadza n’takalamba. -Zokoma zimabwera munthu utatha kale kapena nthawi imene sumayembekezera. Tonde akadula, sabwerera. -Tonde akadula cholinga chake chimakhala kupita komwe kuli matazi. Akawapeza amangoumirira komweko. Chimene mtima wako watsimikiza osaleka mpaka chitatheka. Tsabola wakale sawawa. -Mawuwa amatanthauza kuti malangizo a anthu akale ndi osathandiza. Tsachipenembe anaotcha nkhokwe. -Munthu amene amadziwa bwino mmene zinthu zimakhalira ndi kuyendera ndi amene nthawi zina amabweretsa chipwirikiti. Tsamba likagwa manyazi amagwira mtengo. -Mwana akalakwa manyazi amagwira makolo ake. Makolo akhoza kupeza mavuto chifukwa cha ana awo. Tsata mphero. -Mawuwa amanenedwa pochenjeza munthu kuti angopitira kukapera ufa, osati kukanena mabodza. 219