Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 218
Miyambi ya Patsokwe
Tambala n’tabwali, amamasula tambwali mnzake.
-Ukafuna kugwira mbala umafunika kutuma mbala inzake.
Tambala salira kwa eni, amalira kwawo.
-Munthu sungakhale mfumu kwa eni, koma kwanu.
Tangovutika, opanirira mphika ali chete.
-Nthawi zambiri anthu amene amagwira ntchito yolemetsa ko-
manso yokhetsa thukuta sapeza ndalama zambiri, koma
mabwana awo omwe amangokhala muofesi.
Tapita m’njira adasiya tonse m’khola.
-Tikamadutsa pamudzi wa abale kapena anthu owadziwa
tiyenera kumakawaona kuti ali bwanji, chifukwa tikhoza ku-
wadutsa iwo ali m’mavuto kapena asakupeza bwino.
Tatuma chitsiru kuti chimange mtembo.
-Mawuwa amanenedwa anthu akamadandaula kuti munthu
amene anamutuma kuti agwire ntchito inayake wailephera
kapena wachita zokhumudwitsa.
Tentha tizime adapsetsa anzake.
-Mawuwa amanena za munthu amene ankauza anzake kuti
ayatse moto ndipo auzimitsa pamapeto pake n’kupezeka kuti
waotcha anzakewo. Anthu ena amaputira anzawo mavuto chifu-
kwa cha khalidwe lawo loipa. Mwachitsanzo, bambo wokonda
mowa amachititsa kuti ana ake avutike.
Thendo limakoma, nyama kulowa m’mano.
-Masamba otendera amakoma. Komabe nyama ndi yokoma
kwambiri koma kulowa m’mano. Ukafuna zokoma umafunika
kudziwa kuti zili ndi zowawa zake.
Thumba la Tambe amamasula ndi Tambe yemweyo.
-Munthu akakhala kamberembere amene amadziwa khalidwe
lake ndi kamberemberenso. Tambwali akamanga thumba,
217