Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 217

Miyambi ya Patsokwe Taleka m’talawa adatha mphika. -Munthu akazolowera kuchita chinthu amafika polephera ku- chisiya. Mwachitsanzo, ukayamba kuchita zoipa umazolowera n’kuyamba kuvutika kuti usiye. Taleka ndiyese anakwatira mkazi wa mfumu. -Tisamataye mtima msanga ngati tikufuna zinazake chifukwa nthawi zina zosatheka zimatha kutheka. Talemberana chimfine. -Kulemberana chimfine ndi kupatsirana chimfinecho. Anthu an- gapatsirane chimfine ngati ali malo amodzi. Choncho, mawuwa amanthauza kuti anthu akumana pamodzi pachibale kapena anakumana kuti akambirane zinazake. Tambala adalipira fundudwa. -Munthu ukamayenda ndi wina wokonda zoipa tsiku lina umadzalipira chifukwa cha zolakwa zake. Tambala akavumbwa akunga nsoti. -Tambala akanyowa nthenga zake zimamatirira kuthupi lake moti amangooneka ngati kankhuku kakang’ono. Chimodzimodzi munthu wamkulu akachita zopusa anthu amasiya kumulemekeza. Tambala akavumbwa sayenda malonda. -Tambala akanyowa nthenga zake zimamatirira kuthupi lake moti amangooneka ngati kankhuku kakang’ono. Utamugulitsa sangayende malonda chifukwa amaoneka ngati nkhuku yaing’ono. Chimodzimodzi munthu wamkulu akachita zopusa anthu amasiya kumulemekeza. Tambala amakula kwawo, kwa eni n’chipsolopsolo. -Ngakhale kwanu utakhala wolemekezeka, ukakhala kuchilendo umafatsa. 216