Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 216
Miyambi ya Patsokwe
Sunga khosi, mkanda uwoneka.
-Munthu amafunika kupirira komanso kudziletsa kuti adzapeze
zabwino m’tsogolo.
Suntche adati, “Pita pansi ukamve.”
-Osamamvera zilizonse zimene anthu akunena. Kumatsimikizira
kaye ngati zilidi zoona.
Suzi suzi, alimba ndi mbalame zake.
-Munthu ukatchera msampha umasuzumira kuti uone ngati
wagwira kanthu. Ndi bwino kumayang’ana kawirikawiri chin-
thu chomwe tikuyembekezera.
Suzumire adaphetsa mkhalakale.
-Mbalame ina yomwe inkhakhala kuphanga sinkasuzumira pan-
ja kuopa kuphedwa. Tsiku lina inzake inabwera kudzakhala
nayo ndipo mbalameyi inalangiza inzakeyo kuti isamasuzumire
panja ikamva phokoso. Koma mbalameyi sinamvere moti inasu-
zumira ndipo anthu ataiona anaipha pamodzi ndi inzake ija.
Munthu wina akalakwa n’kumafufuzidwa amapezeka kuti ag-
widwa ndi ena amene anabisala n’kulangidwira limodzi. Ku-
chenjeretsa kapena kusaugwira mtima kumabweretsa mavuto
ngakhale kwa anthu ena aphee.
215