Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 215
Miyambi ya Patsokwe
Si mbewu yoisunga.
-Mawuwa amanenedwa akamafotokoza za anthu ovuta kapena
ana ovuta. Anthu ena akakwiya amanena mawuwa potanthauza
kuti anthuwo ndi amphulupulu omwe sangawasunge pakhomo.
Sikadza kokha kaopa kulaula.
-Kuti munthu atukuke kapena apeze chimene akufuna amafu-
nika kugwira ntchito mwakhama.
Sikadza kokha, kaopa kulaula.
-Ngati munthu akusowa chinthu ayenera kupita kukachifunafu-
na chifukwa sichingamupeze pamene wakhalapo.
Sikuli komire kwa apongozi.
-Pachikamwini sipamafunika ulesi. Umafunika kugwira ntchito
mwakhama m’malo modalira apongozi, chifukwa akatopa nawe
akhoza kukuthamangitsa.
Simbwesimbwe ananya chiwindi.
-Munthu wochita zinthu kuti ena amutamande amadzakhaula
tsiku lina.
Sindinazione anachezera kuziona.
-Pali zinthu zina zomwe zingakhala bwino kuti usakumane nazo
kapena usayambe kuzichita chifukwa ukangoziyamba siziku-
choka.
Suku laliwisi silichedwa kukonyoka ndi mphepo.
-Ana akakumana ndi mavuto samalimba. Zimene akumana nazo
zikhoza kusokoneza tsogolo lawo lonse.
Sunga khosi, mkanda woyera udzavala.
-Munthu amafunika kupirira komanso kudziletsa kuti adzapeze
zabwino m’tsogolo.
214