Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 214
Miyambi ya Patsokwe
Saweruzika adamera nyanga pamphumi.
-Nyama ina inauzidwa kuti kukagwa chilala nyanga zim-
apangitsa kuti nyama izilephera kumwa madzi. Koma iyo
sinamvere ndipo inameradi nyanga pachipumi. Chilala chi-
tabwera inafa ndi ludzu chifukwa imati ikati imwe, nyanga zija
zinkapezeka kuti zagunda pansi. Kumvera kumathandiza kuti
tisakumane ndi mavuto oopsa.
Saweruzika anamanga nyumba pamwala.
-Munthu amene amadziyesa wodziwa zonse amalephera kufun-
sa ena mapeto ake, amalakwitsa anthu n’kumuseka. Ndi bwino
kumafunsa ena.
Sayenda adabala mwana adayenda.
-Usamachitire ena choyipa ngakhale iweyo suyenda chifukwa
nthawi ina amadzayenda ndi mwana wako ndipo anthu una-
wanyozawo amadzachitira choipa mwana wakoyo pobwezera
zimene iwe unawachitira.
Sayenda anabala mwana nayenda.
-Tisamanyoze anthu amene amaoneka monyozeka chifukwa
tsiku lina amadzachita zinthu zomwe sitimayembekezera.
Sekerera cha nkhama, cha mano chiluma.
-Zinthu zikamakuyendera, nthawi zina ndi bwino osasekerera
(kusekerera cha nkhama) chifukwa ena akakuona sasangalala.
Mwachitsanzo, kumangouza anthu kuti wagula wailesi
kungachititse kuti akubere.
Sekeserani, kumtondo kwanka ana, Sakhwi watsala yense.
-Kusekesera ndi kusefa ufa. Munthu amanena mwambiwu aka-
mauza mkazi wake kuti sanakhute, ndiye aphikenso chakudya
china.
213