Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 213

Miyambi ya Patsokwe Safunsa adamanga nyumba pamchenga. -Munthu amene safuna kumva malangizo a ena amachita zinthu zopanda nzeru monga kumanga nyumba pamchenga. Safunsa adanka ndi zoipa pabwalo. -Munthu yemwe samafunsa ena amatha kuchita kapena kunena zinthu zomwe zikhoza kumuika m’mavuto. Safunsa adapita kumanda. -Kufunsa ena kumathandiza kuti tisalakwitse. Safunsa adataya mwana. -Munthu wina ali paulendo anasungitsa mwana wake kwa an- thu ena. Iye sanaganize zowafunsa kuti kwawo ndi kuti. Kenako anthuwo ananyamuka n’kumapita ndi mwana yemwe uja. Mun- thuyo anasowa kolowera chifukwa sankadziwa kuti angakawa- peze kuti. Munthu amene safunsa amatha kuwonongetsa zinthu zambiri. Safunsa adatenga njira ya kumanda. -Kufunsa ena kumathandiza kuti tisalakwitse. Safunsa adaviika nsima m’madzi. -Mwana wina anapatsidwa mtolo wa luzi kuti akauviike m’madzi. Iye sanafunse kuti amuuziranji zimenezo, choncho anangoviika n’kumabwerako. Atafika anthu anamufunsa kuti, “Wadya nsima ija?” Iye anayankha kuti, “Ayi.” Anamuuza kuti chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, anamuikira nsima mu luzimo kuti akadyere kwina. Ndiye chifuka choti sanafunse anakaiviika m’madzi. Kufunsa zinthu si kupusa. Safunsa anamangira nsima mumtolo. -Kufunsa zinthu si kupusa. Munthu umatha kuzindikira kapena kudziwa njira yochitira chinthu ukafunsa. 212