Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 210

Miyambi ya Patsokwe Phukusi la moyo sakusungira ndi mnzako. -Munthu wamantha amakhala zaka zambiri ndi moyo chifukwa manthawo amamuthandiza kuti asamachite mphulupulu zom- we zingachititse kuti afe msanga. Phuliphuli ndi penti, njinga ndi tcheni. -Kumayang’ana mumtima m’malo mopusitsika ndi maon- ekedwe akunja. Maonekedwe amapusitsa. Phwiti akakhuta salawira mtondo. -Pali anthu ena ukawachitira zabwino amangoti zii, osayamikira zimene wawachitira. Amaoneka akakhala kuti akufuna chinachake basi. Anthu akakulandira bwino pamalo umafunika kuwathokoza m’malo mongonyamuka ngati ukutuluka m’chimbudzi. Phwiti akatha kudya amangouyamba n’kumapita. Piringupiringu ngwa njuchi, yoluma ndi imodzi. -Pokamba nkhani pafunika kunena zenizeni m’malo momango- zungulirazungulira. Mwambiwu umanenedwanso pakakhala anthu ambiri amene akuganiziridwa kuti alakwa, koma pamapeto pake amapezeka m’modzi. Pita uko si kuyenda koma tiye kuno. -Si bwino pamene muli paulendo umodzi kupangana kuti dzera uko chifukwa pa ulendo wotero pamavuta kukumana kwake. Komanso pophunzitsa munthu zinazake, si bwino kumango- muuza zochita iweyo osachita. Pofera salambula. -Munthu sungadziwe kumene udzafere. Choncho, kukhala bwino ndi ena n’kofunika, ngakhale anthu akutali, kuti ukadzaf- era kumeneko adzakuike m’manda. Pokoma anatayira galu. -Mawuwa amanena za munthu amene ndi wosayenera 209