Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 21
Miyambi ya Patsokwe
Bwato silidya.
-Nsengwa, dengu kapena bwato zimangosunga zinthu zimene
mwaikamo, sizimachepa kapena kuwonjezereka. Tizikhutira ndi
zimene tili nazo pamoyo wathu.
Bwenzi lako ndi la wina.
-Tizichenjera ndi anzathu amene timacheza nawo chifukwa tika-
wauza kathu, iwonso amakauza anzawo.
Bwenzi mkoma uli moyo.
-Pali anthu ena amene amakonda anzawo zinthu zikamayenda,
koma zikavuta amawathawa.
Bwenzi ndi mthanthira, mlamba udaolotsa khoswe.
-Bwenzi lenileni liyenera kukhala lokonzeka kuthandiza mnzake
akakumana ndi mavuto, osangoti pa zabwino zokha.
Bwerera ali konse.
-Mnzako akakuchitira chabwino umafunika kumuthokoza. Ko-
ma iwenso umayenera kudzamuchitira zabwino, asamangochita
yekha.
Bza sapita kawiri.
-Bza ndi mvekero wa kuthawa mwamwayi. Ngati munthu wap-
ulumuka pa vuto mwamwayi, si bwino kubwereza kuchitanso
zomwezo.
20