Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 209

Miyambi ya Patsokwe Pawiripawiri sipauzirika. -Munthu sungapemerere utsi ku mauna awiri a mbewa pa nthawi imodzi. Munthu m’modzi sangachite zinthu ziwiri nthawi imodzi zinthuzo n’kuyenda bwinobwino. Tizichita chimodzi pa nthawi imodzi. Payerepayere fisi anadya mkazi wake. -Tsiku lina fisi anamva njala kwambiri ndipo anadya mkazi wake. Anthu ena akasimidwa amangochita zinthu bola apu- lumuke m’mavuto awo. Anthu oterowo amachita zinthu mwa payerepayere ngati zimene fisi anachita podya mkazi wake njala itavuta. Pendapenda si kugwa koma kuchalira ulendo. -Kulephera sikutanthauza kuti sungakwanitse kuchita chinthu. Kuti munthu achite bwino amafunika kukumana kaye ndi mavuto. Phika mowa kuti umve amene anapha amako. -Pamowa ndi pamene anthu amayankhula zakukhosi kwawo ngakhale nkhani zachinsinsi. Munthu woledzera ndi mwana ndi amene amanenadi zoona akafunsidwa zinthu. Kuti anthu aku- uze zoona zenizeni umafunika kuwanyengerera monga ku- wapatsa chinachake ndipo amasanza nkhani yonse. Phiri siliyendera munthu. -Munthu amene akufuna chinachake ayenera kupita kumene chinthucho chimapezeka. Osamangodikira kuti chikupeza uli pampando khale! Phiri siliyendera nyani. -Munthu amene akufuna chinachake ayenera kupita kumene chinthucho chimapezeka. Osamangodikira kuti chikupeza uli pampando khale! 208