Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 207
Miyambi ya Patsokwe
limodzi zinthu zina monga kudyera limodzi mmemo.
Tizigawana zinthu zimene tapeza limodzi.
Papangano saika mwala.
-Kumakwaniritsa malonjezo ako m’malo moikapo mwala.
Papita mkazi mnzako, nawenso pitapo.
-Nthawi zina ndi bwino kumachita zimene ena akuchita monga
pamaliro ndi malo ena.
Papita mnjere mpeni upita pomwepo.
-Mnjere ndi chakunja cha zipatso ngati mandimu ndi malalanje.
Munthu ukamasenda ndi mpeni, mpeniwo umangodutsa mom-
we chikhungucho chathera. Munthu amalandira chilango malin-
ga ndi zimene wapalamula. Nthawi zambiri munthuyo aka-
kachita apilu, zimapezeka kuti mpeni umadutsa momwe wo-
yamba uja unadutsa.
Papsa tong’ola sudziwa mtima wa moto.
-Ukamawotcha chimanga umafunika kumangodyeratu chifu-
kwa ukapusa chimatha kupserera. Ndi bwino kumagwiritsa
ntchito mwayi ukapezeka chifukwa zamawa sizidziwika.
Pasamba mfulu, kapolonso amasambira pomwepo.
-Munthu ukakhala pantchito, chomwe bwana wako wapeza
monga phindu nawenso umadyerera nawo. Komanso ukakhala
ndi anthu opeza bwino n’kumakhala nawo bwino umadyerera
nawo.
Pathindi Nkhwali, Mkango uli pomwepo.
-Nkhwali ikati itere powirira nthawi zina pamakhalanso pali
Mkango pomwepo. Pamene pali zabwino pamakhalanso
mavuto. Ndi bwino kupirira mavutowo kuti upeze zabwinozo.
Pati bii pali minga.
-Pamene pali ntchire nthawi zambiri pamakhalanso minga.
206