Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 205

Miyambi ya Patsokwe Palibe munthu amasula mfuti nkhondo itafika m’mudzi mwake. -Munthu uyenera kumakhala wokonzeka nthawi zonse kuti udziteteze ku mavuto. Palira mbirira pali khwawa. -Pamene pakumveka madzi pamakhala kuti pali mtsinje kapena khwawa. Mphekesera zikamamveka ndiye kuti chinachake chachitika. Pama loyesera limathyola chala. -Munthu akalakwa pamafunika kumupatsa chilango chomuye- nerera. Tikapereka chilango chankhanza timakhala tiku- lakwiranso munthuyo. Pamalima m’pamimba, khasu la Chidambo. -Kuti munthu agwire ntchito amafunika kudya mokwanira. Pamene wapsa supitapo kawiri. -Pamene munthu wakumana ndi mavuto supitapo kawiri, pokhapokha ngati uli woduka mutu. Pamodzimodzi padawoletsa dzungu. -Munthu amafunika kumayesanso zina. Osamangochita chimodzimodzi chifukwa pamapeto pake sangatukuke. Pamsasa saipitsa. -Ukakhala pamalo achilendo umafunika kuonetsa khalidwe labwino. Komanso ukachokapo si bwino kusiya utasokoneza chifukwa umatha kukumana ndi mvula n’kufunanso utabw- erera kunsasa komwe kuja. Pamudzi pakakhala pa zitsilu, mkamwini asamakulirepo mwendo. -Si bwino kunyoza eni mudzi ngakhale akuoneka opusa, chifu- kwa sudziwa zimene amapangana. 204