Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 204

Miyambi ya Patsokwe Pakamwa podya therere. -Mawuwa amanena za munthu amene amakonda kunena bodza. Pamakhala ngati pakamwa pake mpoterera ndi therere. Pakamwa saphonya. -N’zovuta kulephera kuchita zimene unazolowera. Ngakhale utakhala kuti ukudya nsima mundima, sungaphonye pakamwa. Pakamwa sipayamika, umayamika ndi mtima. -Tiyenera kumayamika anthu akatichitira zabwino, osamango- landira ngati mmene pamachitira pakamwa tikamadya. Pakaphale phwiti sapheka. -Mlandu wa m’bale wako umavuta kuweruza. Pakati pa ine ndi inu pali kanthu. -Mawuwa amanenedwa ngati mukuona kuti pali kusamvana pa- kati pa inu ndi ena. Pakhomo sitichoka ngati tikutuluka m’chimbudzi. -Ukamachoka pamalo umafunika kutsanzika m’malo mon- gochoka ngati palibe amene unawapeza. Pakhota mchira wa nyani. -Mawuwa amanenedwa potanthauza kuti chenicheni sichikud- ziwika, pagona nkhani sipakudziwika. Ngati padziwika amati, “Tsopano tapeza pamene pakhota mchira wa nyani.” Pali chala pali munda. -Kale anthu ankakonda kulozera anzawo kumene kuli munda. Ndiye mawuwa amatanthauza kuti pamene anthu akulozerana ndiye kuti pali chinachake. Mwachitsanzo, ena akamakuuza mavuto ako, umayenera kudziwa kuti n’kutheka kuti palidi vuto. Palibe chinsinsi padziko lapansi. -Ngakhale mutabisa chotani, zinthu zimaululika. 203