Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 203
Miyambi ya Patsokwe
zoipa zomwe zimaoneka ngati zosangalatsa kumabweretsa
mavuto oopsa. Osamakomedwa ndi zinthu.
Pakadapanda Njiri kufera m’dambo, chizimba mukadayesan-
ji?
-Dzino la Njiri ndi mankhwala a khunyu komanso chizimba cha
mankwala ena. Osamapsera mtima munthu amene watithandi-
za, ndi bwino tizimuthokoza.
Pakamwa ndi pa boma, ukasewera napo pakumangitsa.
-Tiyenera kusamala ndi zomwe timanena chifukwa zikhoza
kutiika m’mavuto.
Pakamwa padzaulukira mbereswa.
-Mawuwa amanena za munthu wina amene sanamvetse nkhani
n’kumakauza ena. Anthu akamamudzudzula amamuuza kuti
akamangoyankhulayankhula zomwe sanazimvetse, pakamwa
pake padzaulukira mbereswa.
Pakamwa pakudya zamchere.
-Mawuwa amatanthauza kuti pakamwa pamatha kutuluka
zabwino ndi zoipa zomwe. Munthu akhoza kulakwitsa ponena
zinthu.
Pakamwa palibe m’dima.
-Munthu samaphonya pakamwa ngakhale akamadyera mumdi-
ma, amakhala anapazolowera kwambiri. Munthu sangalephere
kuchita zomwe anazolowera.
Pakamwa pamawombola.
-Anthu amene amadziwa kuyankhula amatha kupulumuka pa
mlandu chifukwa chochenjera pakamwa.
Pakamwa pamodzi sipalawa ndiwo.
-Munthu m’modzi sanganene maganizo oimira anthu onse. Ti-
mafunika kufufuza kwa enanso kuti titsimikizire.
202