Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 201
Miyambi ya Patsokwe
Pachedwa msulu pali nyerere.
-Kumene munthu amakonda kupita kapena chimene aku-
chilimbikira ndiye kuti kuli chabwino chimene akuona kuti
apezako.
Pachoka mnzako pali malo.
-Wina akasiya kuchita zinazake, anzake amapezerapo mpata
wochita zinthuzo.
Pachulu ndapaleka, ana a mbuzi angasewerepo.
-Pachulu ndi pamene anthu amakonda kudzalapo ndiwo za-
masamba chifukwa zimabereka bwino. Mawuwa amanenedwa
munthu akasiya kuchita zinazake poopa kuti zingowonongeka.
Pachulu palibe chiphe.
-Anthu ena otchuka amakhala okoma mtima, koma pali ena
osadziwika kwambiri omwe amakhala oipa mtima.
Padiwa sasewera.
-Tisamachite zinthu zomwe zikhoza kutiika m’mavuto.
Padutsa khasu sipanama.
-Kuchita khama pantchito kumabweretsa phindu.
Mwachitsanzo, munthu amene wachita khama kulima sabwera
chimanjamanja.
Padyera mfulu, kapolo amadyera pomwepo.
-Mnzako akakhala pabwino iwenso umadya nawo zimene
amapeza.
Padzikoli mpongoothera dzuwa, tikaothaotha timachokapo.
-Moyo ndi waufupi, siuchedwa kutha. Umangokhala ngati una-
badwa kuti udzaothere dzuwa kenako n’kuchokapo.
Padziwa ndi pansi mwana wa mfuko akadwala.
-Munthu wina akakuchitira chipongwe n’kuthawa, anthu
amanena kuti, “Ingomulekani, akadzapezeka tidzaona naye
200