Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 20
Miyambi ya Patsokwe
Bodza lilibe mwini.
-Anthu amene sitimayembekezera kuti anganame nthawi zina
amanena bodza m’maso muli gwa.
Bodza limabwerera mwini wake.
-Munthu ukanena bodza, bodzalo limakusakasaka mpaka ku-
kupeza. Ndi bwino kumasamala ndi zimene timanena, ngati til-
ibe nkhani ndi bwino kungokhala chete m’malo momapeka ma-
bodza.
Bololo sakonda madzi.
-Pamene munthu watsimikiza kuchita kanthu kena, amakumana
ndi mavuto komanso mayesero. Komabe, sayenera kulola kuti
zimenezi zimulepheretse cholinga chake kapena kumugwetsa
mphwayi.
Bongololo anali ndiwo, timadya ndi a uje.
-Si bwino kumadzitama pa zinthu zomwe sunapange chifukwa
nthawi zina umangonama kuti unapanga.
Bongololo sadzolera mafuta pagulu.
-Si bwino kuulula zinsinsi zathu zonse, pali zinthu zina zomwe
sitiyenera kuuza ena monga zam’banja. Nthawi zambiri munthu
akaulula zimenezi amayalutsa banja lakelo.
Bonongwe mkoma akadadza.
-Nthawi zina mlendo amaonetsa makhalidwe abwino, koma
akakhalitsa amaonetsa khalidwe lake lenileni.
Buluzi kuthandiza mbewa kuthawa.
-Nthawi zina anthu amene sitigwirizana nawo kapena amene
sitiwadziwa ndi amene amatithandiza.
Buluzi wa ize (mnyengo) anapanidwa ndi chitseko.
-Kuchita zinthu zachinyengo monga chiwerewere kapena kuba
kukhoza kutiika m’mavuto osaneneka.
19