Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 199

Miyambi ya Patsokwe Osamayankhula za kuntchini kwadzadza. -Osamayankhula zinthu zopanda nzeru kapena zimene aliyense akuzidziwa kale. Kapena kumanena zinthu zoti anthu akudziwa kale. Nanga ndi ndani amene sadziwa kuti kuntchini kumadza- dza? Osamayenda monyang’wa ngati supita kuchimbudzi. -Anthu tonse ndi ofanana. Tisamachite matama chifukwa cha zinthu kapena udindo umene tili nawo. Tonse ndi anthu ofanana. Osamayerekedwa ngati supita kuchimbudzi. -Aliyense ndi munthu ndipo zimene timafunika kuti tikhale ndi moyo n’zofanana. Tisamawalire anzathu ngati tili ochita bwino kapena ngati tili ndi luso lina, chifukwa tonse ndi anthu basi. Ngakhale nkhuku ataidula mutu, singaganize choncho! -Mawuwa ndi okokomeza osonyeza kuti munthuyo sanaganize bwino mpang’ono pomwe. Amayerekezera kuti ngakhale Nkhuku itaduka mutu sigaganize choncho. Osamwa mankhwala oyenera kupakidwa pachilonda. -Kusemphanitsa zinthu. Mawuwa amachenjeza munthu amene akufuna kuchita zinthu mopupuluma asanamvetse bwinobwino zonse. Osanditengera ku mtoso ngati maliro a njoka. -Mawuwa amatanthauza kutenga njoka yakufa yomwe sukufu- na utaikhudza ndi kamtengo kotosera zomwe zimatanthauza kunyoza. Tisamanyoze anzathu koma tizilemekezana. Osanditengera ku mtoso ngati nyama ya galu. -Mawuwa amatanthauza kutenga nyama yagalu yomwe sukufu- na utaikhudza ndi kamtengo kotosera zomwe zimatanthauza kunyoza. Tisamanyoze anzathu koma tizilemekezana. 198