Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 198

Miyambi ya Patsokwe Osamafunsa za fungo m’chimbudzi. -Mawuwa amanena za munthu amene akufunsa zinthu zoti aku- zidziwa kale. Ndani angakhale pansi n’kumafunsa ngati ku- chimbudzi kumanukha kapena ayi? Osamagenda kupolisi chamba chili m’thumba. -Kupalamula ukudziwa kuti uli ndi milandu ina. Osamagulitsana makasu othyoka. -Tisamachitirane zinthu zopanda chilungamo kapena kupusitsa anzathu. Osamaluma dzanja limene limakuthandiza. -Osamanyoza kapena kuchitira chipongwe amene amakuthandi- za. Osamanyerera pambali pam’boo ukupaona. -Osamachita zoipa, zabwino ukuzidziwa. Mwachitsanzo, ena akakuuza malangizo oyenera oti uchitire zinazake iwe n’kuchita zosiyana ndi zimenezo, umakhala ngati wanyerera pambali pam’boo ukupaona. Osamasambira molimbana ndi madzi, angakutenge. -Si bwino kumachita zinthu zosiyana ndi zimene ena akuchita chifukwa mapeto ake umatha kukumana ndi mavuto. Munthu amene akusambira n’kumalimbana ndi madzi, amatopa ndipo madziwo amamutenga. Osamasewera paulimbo. -Pali zinthu zina zomwe zikhoza kuwononga moyo wathu. Ndi bwino kupewa zinthu zimenezo m’malo momachita masewera n’kukumana ndi mavuto ngati mmene mbalame imachitira ika- khala kuti imasewera ndi ulimbo. Osamatsinira mafulufute kuuna. -Osamachita zinthu zomwe zingatsekereze mwayi. 197