Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 195

Miyambi ya Patsokwe Nyenderera zidatha kakule. -Munthu akamachita zinazake mobisa, n’kupita kwa nthawi amalephera kuzisiya. Nyimbo imodzi sachezera gule. -Kusinthasintha zinthu kumathandiza. Nyundo m’masulano. -Nyundo ndi hamala. Nyundo imathandiza kuti chigwandali chikhale mpeni. Ndi bwino kumathandizana. Nyumba imayamba ndi njerwa imodzi. -Zinthu zikuluzikulu zimayamba ndi zing’onozing’ono. Nyumba ya chitsiru siipsa. -Nthawi zina pooneka ngati wopusa, umapewa mavuto ambiri. Nyumba ya mwini saotchera mbewa. -Munthu wina ankatenthetsa madzi oti akawaze m’nyumba kuti aphe mphutsi. Mlendo wake ankaganiza kuti akuphika msima moti anaotcha mbewa zake. Anadikirira koma nsima sinabwere. Osamadalira zinthu za ena tikamachita zinthu monga kukwatira tikuganiza kuti makolo adzatithandiza. Nyumba yabwino imakhala ndi moto. -M’nyumba kuti mukhale mosangalatsa muyenera kukhala zin- thu zofunika monga zakudya. Nzeru ndi chuma. -Munthu wanzeru ndi amene amatukuka komanso kukhala moyo wabwino. Nzeruzayekha adaviika nsima m’madzi. -Ngati tikukayika kapena sitikudziwa zoyenera kuchita ndi bwino kufunsa kuti tichite zinthu moyenera. 194