Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 194

Miyambi ya Patsokwe Nyalugwe mchepsa kanzake, mkuzakake akapha chiwala achi- ta chokoka. -Pali anthu ena omwe safuna kuyamikira zochita za anzawo, ko- ma zawo ngakhale kang’onong’ono amadzitamandira. Nyama ya liuma inafa ndi ludzu. -Nyama ina inkakakamira kuikidwa nyanga zazitali. Chilala chi- tafika, madzi anayamba kusowa moti nyama zina zinkamwa kumphanga. Nyamayo inafa ndi ludzu chifukwa cha nyanga zake zazikulu zina. Kukula mtima, kusamva za ena kapena mwano zimabweretsa mavuto. Nyama yokoma idadza mano atantha m’kamwa. -Anthu ena akamabwekera nyama amanena mawu amenewa. Nyama yokoma idadza n’takalamba. -Anthu ena akamabwekera nyama amanena mawu amenewa. Nyambo m’masiku, chimawerenga ndi chitseko. -Mawuwa amanenedwa wina akamachenjeza mnzake kuti ti- dzaona m’tsogolo chifukwa masiku sachedwa kutha. Nyang’anyang’a amapulumutsa. -Kuyenda kapena kuchita zinthu mwachifatse kumapulumutsa munthu m’zambiri. Nyani samulekera munda. -Si bwino kusiya kuchita chinthu chifukwa cha munthu wina woononga kapena amene akufuna kukusokoneza. Nyau imakoma n’kuwala. -Kuti mkazi kapena ana azioneka bwino umafunika kuwaveka zovala zabwino. Chinyau ndi chosaoneka bwino, koma kuchipa- ka zina ndi zina kapena kuchikongoletsa chimayamba kuoneka bwino. 193