Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 193
Miyambi ya Patsokwe
Ntchenzi idamva mawu oyamba.
-Munthu wina ananena kuti, “Nditchera msampha mawa,” ke-
nako anasintha n’kunena kuti lero. Ntchenzi inangomva mawu
oyambawo ndipo inabwera n’kugwidwa. Tizichenjera
tikamanena zinthu chifukwa anthu amagwira mawu anthu
oyamba.
Ntchenzi m’mbuyo.
-Mawuwa amanena za munthu wabodza. Anthu amanena
mawuwa pofuna kuchenjeza anzawo kuti achenjere, wama-
bodza akubwera.
Ntchito ndi mumtengo.
-Munthu ukakhala pantchito uyenera kukhala mosamala ngati
mmene umachitira ukakwera mumtengo chifukwa nthawi ili-
yonse ikhoza kutha, ukhoza kutsakamuka.
Ntchito siichepa.
-Ntchito ingakhale yonyozeka tiyenera kuigwira mosamala ko-
manso mwakhama.
Ntchito zimatsata msinkhu.
-Munthu wamkulu sayenera kumachita zibwana.
Nthawi siidikira munthu.
-Kaya ukutani, nthawi simayembekezera kuti uchite kaye zim-
enezo, imangopitabe.
Nthunzi sufuka pachabe.
-Nkhani simangomveka, pamakhala kuti pachitika chinachake.
Nyalugwe m’chepsa chamnzake, iye akapha chiwala achita ku-
koka.
-Pali anthu ena okonda kunyoza za anzawo koma amakometsa
zawo ngakhale zitakhala zosalongosoka.
192