Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 192
Miyambi ya Patsokwe
chifukwa cha khalidwe lake loipa.
Nsomba ikaola imodzi, zaola zonse.
-Pamudzi munthu akakhala wamakhalidwe oipa monga waku-
ba, anthu amangoti mudzi wonse ndi wa anthu akuba ngakhale
wakuba ali m’modzi yekha. Kulakwa kwa munthu wina kukho-
za kukhudza anthu ena.
Nsomba ndi therere saphika mphika umodzi.
-Nkhani kapena zinthu zosiyana si bwino kuzikambira pamodzi.
Chilichonse chiyenera kuonedwa pachokha.
Nsungwi yantuwa sisiriridwa.
-Nsungwi yantuwa ndi yosakhwima. Palibe munthu amene an-
gaidule kuti akachitire chinachake chifukwa imakhala yosalim-
ba. Munthu akakhala waulesi amuna kapena akazi samufuna.
Munthu azionetsa chamuna.
Nsupa ndi nsupa, mulibe thonje.
-Munthu amadziwika ndi khalidwe lake. N’zoona kuti tonse ndi
anthu, koma timasiyanabe zochita. Makhalidwe abwino
azionekera poyera.
Ntchembere yamapasa izigona chagada.
-Ukakhala pakati umaona mbali zonse ziwiri n’kumapereka
thandiza kumene kukufunikira.
Ntchentche inati, “m’tsogolo moyo, m’mbuyo moyo.”
-Si bwino kumachoka pamalo utaipitsapo chifukwa tsiku lina
udzafunanso kubwererapo.
Ntchentche yadyera inapita ndi maliro kumanda.
-Munthu wotengeka ndi zilizonse amataika n’kukumana ndi
mavuto.
Ntchentche yojijirika inaphinjidwa ndi nchimba.
-Si bwino kukhala anthu ojijirika, tingakumane ndi mavuto.
191