Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 191
Miyambi ya Patsokwe
Nsapato imodzi savala anthu awiri.
-Anthu angapo sangakhale pa udindo umodzi.
Nsengwa siidya.
-Nsengwa, dengu kapena bwato zimangosunga zinthu zimene
mwaikamo, sizimachepa kapena kuwonjezereka. Tizikhutira ndi
zimene tili nazo pamoyo wathu.
Nsengwa ya muyeso amathyola ndi anansi.
-Nthawi zina anthu amene amakhala adani athu chifukwa
chowononga zinthu zathu amakhala achibale kapena ena apa-
fupi.
Nsengwa ya nsima savundikira ndi chikho.
-Timafunika kusamala zinthu zathu pozisunga pabwino kuti
zisawonongeke.
Nsengwa yobwereka samangira banja.
-Kuti munthu akwatire kapena achite zinazake amafunika ku-
konzekera m’malo momadalira zinthu za ena.
Nsikidzi zikalumaluma zimalowa m’tsekera.
-Mawuwa amanena za anthu omwe amati anzawo akawachitira
zabwino amangozimiririka osathokoza.
Nsikidzi zinachilira kwa alendo.
-M’nyumba anthu akhoza kukangana koma kukabwera alendo
anawaonetsa chikondi komanso amaoneka ngati ogwirizana
ndipo nthawi zina mkanganowo umathera pomwepo.
Nsima ya apongozi sasungira mlendo, ngakhale yochokera
kwa apongozi.
-Apongozi monga makolo, umayenera kuwapatsa ulemu
waukulu.
Nsomba ikawola imodzi, zonse zawola.
-Munthu m’modzi wosokoneza amaipitsa mbiri ya anthu ambiri
190