Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 190
Miyambi ya Patsokwe
Nsabwe yoyendayenda inakumana ndi chala.
-Munthu woyendayenda salephera kupalamula.
Nsalu ndi kukhosi.
-Aliyense ali ndi ufulu wosankha chimene chamukomera
kapena chimene akufuna kuchita.
Nsalu ya “lekaleka.”
-Mawuwa amatanthauza mwana. Nthawi zambiri ana ama-
konda kugwiragwira ndipo mayi awo angamawaletse kuti
aleke. Akakhala wakhanda, mayi salola kuti aliyense amunya-
mule poopa kumukhonyola. Amauza munthuyo kuti aleke.
Nsalu yobwereka silimba m’chiuno.
-Zinthu zobwereka zimakhala zosadalirika, choncho ndi bwino
kumasamala chimene wabwereka kuti ukachibweze chili bwino.
Nsalu yobwereka sithetsa usiwa.
-Kubwereka zinthu kwa ena si njira yothetsera umphawi koma
kugwira ntchito kuti tipeze zimene tikufuna.
Nsangala za pamaliro ngati matenda adakazonda.
-Kujijirika pa zinthu zoti wapeza zothaitha kapena zochitidwa
kale, pomwe poyamba unalibe nazo chidwi.
Nsanjikizo udaphetsa Kunda.
-Kunda ndi mbewa. Kunda ankasunga zinthu zambiri zomwe
tizilombo tina timafuna kudya nawo. Kunda anayamba kulim-
bana ndi tizilomboto mpaka anaphedwa. Tizipewa kuchita zin-
thu zomwe zingatibweretsere mavuto. Dyera si labwino, lima-
bweretsa mavuto.
Nsanza zili ndi ntchito.
-Si bwino kumawononga zinthu zakale monga chikhalidwe cha
makolo chifukwa chimakhalabe ndi ntchito.
189