Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 19

Miyambi ya Patsokwe Bango likauma, limabwera linzake. -Anthu sasangalala ndi munthu wovuta kapena woipa. Mwachitsanzo, mwana akakhala wamwano kapena wosamvera, makolo ake anganene kuti, “Olo atamwalira, tidzabereka wina.” Banja lili ngati mzinda wozunguliridwa ndi adani, ena amafu- na atalowamo, pomwe ena amafuna atatulukamo. -Munthu amene sali pabanja amafuna atalowa m’banja, koma amene ali pabanja, akaona zokhoma za m’banjamo amafuna atalithawa. Ndi bwino kumayamba taganiza mwakuya komanso kusankha bwino tikamafuna kulowa m’banja. Banja ndi anthu awiri, wachitatu ndi wosokoneza. -Pabanja sakhala anthu atatu. Ndi bwino kukhala ndi wachikon- di m’modzi. Banja ndi gombe, silichedwa kugumuka. -Mawuwa amanena za banja kapena ubwenzi umene umayamba chifukwa cha katundu kapena chuma. Nthawi zambiri zinthuzo zikatha, ubwenzinso umathera pomwepo, si nanga munthuyo amakhala anakwatira kapena anali pa ubwenzi ndi chumacho! Batani lapansana amakumanga ndi mnzako. -Pali zinthu zina zomwe zimafuna mnzako kuti akuthandize. Bemberezi adziwa nyumba yake. -N’zosatheka kuti munthu aiwale kwawo. Bisani matenda, maliro tidzamva. -Munthu utha kubisa mavuto ako aang’ono, koma akafika poipa kwambiri, umafuna anzako kuti akuthandize. Bodza likhoza kuyenda n’kuzungulira theka la dziko lonse lapansi, choonadi chikuvalabe nsapato zake kuti chilitsatire. -Bodza limafala mofulumira kusiyana ndi choonadi. 18