Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 188
Miyambi ya Patsokwe
Nkhuku imalemekezeka ndi nthenga zake.
-Munthu amalemekezeka chifukwa cha khalidwe komanso zo-
chita zake.
Nkhuku yanjiru simaswa mazira.
-Nsanje simapindulitsa munthu. Umafunika kulimbikira ntchito
m’malo momangokhalira kulimbana ndi anzako omwe ziku-
wayendera.
Nkhuku yoweta sagula pamsika.
-Mkazi wabwino samakapena koyenda.
Nkhululu yatcheru ndiyo imaimba lokoma pachilimwe.
-Pa nthawi ya dzinja, Nkhululu imatolera zakudya n’kukasiya
kuuna ndipo simadzavutika m’chilimwe. Tizichita zinthu zom-
we zidzatithandize m’tsogolo.
Nkhuni imodzi siipanga mtolo.
-Munthu payekha sangakhale ndi nzeru zonse, umafunika
kumva maganizo a ena.
Nkhuni imodzi siipsetsa mphika wa nyemba.
-Munthu payekha sangakhale ndi nzeru zonse, umafunika
kumva maganizo a ena komanso kulola kuti akuthandize.
Nkhunzi yamwini sang’ambira khola.
-Munthu sangakulitse khola lake chifukwa cha tonde kapena
ng’ombe yamwini. Tizidalira zanthu osati za eni.
Nkhunzi yobwereka samangira khola.
-Si bwino kudalira chinthu chobwereka chifukwa mwini wake
akhoza kuchifuna nthawi iliyonse.
Nkhutukumve.
-Mawuwa amatanthauza munthu wosamva, amene amangochi-
ta zake.
187