Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 187
Miyambi ya Patsokwe
Nkhani ndi kamnyamata.
-Kucheza sikutha, nkhani zikayamba zimabwerabe zina. Ndi
bwino kumaona polekezera kucheza kuti tizigwira ntchito.
Nkhani siidzala mtanga.
-Kucheza sikutha, nkhani zikayamba zimabwerabe zina. Ndi
bwino kumaona polekezera kucheza kuti tizigwira ntchito.
Nkhani siikalamba.
-Kucheza sikutha, nkhani zikayamba zimabwerabe zina. Ndi
bwino kumaona polekezera kucheza kuti tizigwira ntchito.
Nkhani yalowa m’chala.
-Anthu ena amapondereza nkhani chifukwa choti wolakwayo
ndi m’bale wawo kapena wawapatsa chiphuphu. Zikatere timati
nkhaniyo yalowa m’chala.
Nkhokwe imalimba ndi mphanda.
-Munthu aliyense amafuna wina woti azimuthandiza. Kudali-
rana n’kofunika.
Nkhondo kadzikumbire.
-Nthawi zina pofuna kupezetsa ena mavuto, timapezeka kuti ta-
wavala mavutowo n’kukhaula nawo. Kutchera msampha kuti
wina akodwe, n’kupezeka wakodwa wekha.
Nkhondo ndi anansi
-Amakuchitira choipa nthawi zina ndi abale ako kapena amene
umakhala nawo pafupi.
Nkhonya ya “mudandiyambakale” idagwa m’chikope.
-Mkwiyo ndi woopsa. Kusunga chidani kumachititsa kuti mun-
thu uchite zoopsa kwambiri.
Nkhope ya muthu imanola khope inzake.
-Munthu amathandiza mnzake kuti azichita bwino.
186