Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 186
Miyambi ya Patsokwe
Njuchi zikachuluka siziika.
-Anthu akachuluka pamalo kapena pantchito, zinthu siziyenda.
Aliyense amangosiira mnzake.
Njuchi zikachuluka zilibe usinda.
-Anthu akachuluka pamalo kapena pantchito, zinthu siziyenda.
Aliyense amangosiira mnzake.
Njuchi zingalume, koma ine phula nditenga.
-Kuti upeze zabwino umafunika kulimba mtima komanso
kupirira mavuto. Kuti munthu afule njuchi n’kutenga malesa,
njuchi zina zimamuluma koma iye sagonja mpaka atatenga
uchiwo.
Nkhali imafuna mafuwa.
-Aliyense amafuna wina woti amuthandize.
Nkhali yodikirira imachedwa kuwira.
-Chilichonse chili ndi nthawi yake, ndi bwino kumadikira.
M’malo mongokhala ndi bwino kumachita zina kuti usaone
kuchedwa.
Nkhanga ikakula, siikhala paphira.
-Munthu ukakula umayenera kusiya chibwana.
Nkhanga yaikulu saweta.
-N’zovuta kusintha Nkhanga yaikulu kuti ikhale yoweta. Mun-
thu amene wakula ndi zizolowezi zoipa amavuta kumusintha.
Nkhanga zinapangana kusanaspe.
-Ndi bwino kumaganizira zimene tingachite mavuto atatigwera,
kusiyana n’kumakhala pansi kuti tidziwe chochita mavutowo
akatipanikiza.
Nkhani ndi kamchira, umafunika uyang’ane kaye pali mutu
wake.
-Kumafufuza chimene chachititsa vuto.
185