Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 185
Miyambi ya Patsokwe
Njira salimbira, chikakula patuka.
-Pali zinthu zina zomwe sitingalimbane nazo, zoterozo zimafuna
kungozisiya.
Njira ya kwa amfumu siiwirira.
-Nkhani zonse zofunika kwambiri kaya ndi za maliro, zima-
yenera kukanenedwa kwa amfumu kuti akuthandizeni.
Njira zonse sizipita pamutu pako.
-Nthawi zina ndi bwino kulola kuti zinthu zina zitipite.
Njiwa sasosolera pamsampha.
-Ukasosolera njira pamsampha, zinzake zimadziwa, n’kuchenje-
ra. Tisamaulule zinthu zomwe tikudziwa kuti zikhoza kupereka
mphamvu kwa ena kuti atilange.
Njoka ndi njoka, singasinthe manga.
-Munthu woipa ndi woipa, sangasinthe ngakhale mutamulangi-
za bwanji.
Njoka yopusa imalumira kumchira.
-Pali anthu ena ooneka opusa, anthuwa sitimadziwa zimene
akuganiza kusiyana ndi ena omwe akungolongolola.
Njovu idagwa m’mbuna mwa Aonenji.
-Munthu aliyense ali ndi mwayi wake. Choncho, si bwino ku-
ganiza kuti anthu ena ooneka onyozeka sangapeze mwayi.
Njovu inatuma nyerere.
-Mawu onena moseka omwe ena amagwiritsa ntchito ak-
amatuma mwana kapena munthu wonyozeka.
Njuchi yako ndi iyo yaluma.
-Osamangotsata zinthu zomwe ulibe nazo umboni. Kumatsata
zinthu zenizeni.
184