Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 182
Miyambi ya Patsokwe
kutchukako sikuchedwa kutha. Zikamakuyendera bwino kwam-
biri dziwa kuti zikhoza kukusokonekera.
Ng’ombe ya mnzako sumaiitana.
-Tisamale ndi zinthu za ena kuti nawonso asamale zinthu zathu.
Ng’ombe yaukali imagwa m’mbuna.
-Munthu ukakhala waukali, anthu samakuchenjeza ngati pena
pali zoopsa chifukwa amaopa kuti uwakalipira. Munthu wofatsa
ndi amene amathandizidwa ndi ena.
Ngakhale chitsiru nachonso chili ndi amake.
-Aliyense anganyanse bwanji, angaipe bwanji, amakhala ndi
abale ake komanso anthu amene amamukonda.
Ngakhale matako atafunitsitsa bwanji, sangakhale kutsogolo.
-Pali zinthu zina zomwe sitingakwanitse kuchita ngakhale titafu-
nitsitsa bwanji.
Ngakhale nkhalango ikamapsa, Birimankhwe sasintha
mapondedwe.
-N’zovuta kusintha zimene unazolowera.
Ngakhale wapamtima, usamuuze mawu onse akukhosi.
-Mnzako amene umamukhulupirira amakhalanso ndi anzake
moti chinsinsi chimene wamuuza amakauzanso anzakewo
nkhaniyo n’kufala.
Ngaluwe idalira msampha utaning’a.
-Mawuwa amanena za kulephera kupirira vuto litatsala
pang’ono kutha.
Ngati mtengo wauwisi ukuyaka, ndiye wouma ungatani?
-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wolimba kapena amene
amachita bwino zinazake walephera. Ngati zotere zitachitika
ndiye kuti ena omwe si olimba amangogweratu. Zimene zavuta
181