Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 181

Miyambi ya Patsokwe kuchita zinazake n’kutaya mphamvu zake pachabe. Ndiwonetsetse adathetsa nkhosa. -Kuzengereza pochita zinthu kumapezetsa mavuto. Ndodo imodzi siipha njoka. -Mawuwa amanenedwa pofuna kulangiza ena kuti afunika ku- machita zinthu mobwereza osati kamodzi kokha. Ndodo ya ana ndi imene amaphera njoka. -Osamanyoza maganizo a ana. Nthawi zina mnzeru zawo ndi zimene zimathandiza pamavuto, monga njoka ikalowa m’nyum- ba umatha kutenga ndodo yomwe mwana amaseweretsa n’kuphera njoka. Nena chilungamo n’kuthawa. -Nthawi zina munthu ukanena chilungamo anthu amakuda. Ko- ma kunena chilungamo n’kofunika. Choncho, zimakhala bwino kunena chilungamo koma umafunika kusamala chifukwa ukho- za kukumana ndi mavuto. Nena poipa kuti pabwino patuluke. -Munthu ukamafuna kudzudzula choipa umanena ngati nthab- wala kuti nkhaninkhani ituluke n’kukonzedwa. Ng’oma imalira ikaona inzake. -Anthufe timafunikira anthu ena kuti zinthu zitiyendere bwino. Mwachitsanzo, kuti munthu usangalale ndi phwando umafu- nika anzako. Ng’oma silira yokha. -Ng’oma ikamalira ndiye kuti wina akuimenya. Chimodzimodzi munthu, akamadandaula pakakhala kuti penapake pali vuto. Ng’oma yolira bwino sichedwa kung’ambika. -Munthu ukatchuka kwambiri usamadzitame chifukwa 180