Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 180
Miyambi ya Patsokwe
Ndi mwamuna akadya.
-Munthu ayenera kuonetsa chamuna chake pogwira ntchito
osati pakudya pokha.
Ndi mwamuna pakudya pokha.
-Munthu ayenera kuonetsa chamuna chake pogwira ntchito
osati pakudya pokha.
Ndikanadziwa ndikanaphika therere.
-Mkazi wina ankayembekezera kuti mwamuna wake abweretsa
nyama kuchokera ku uzimba. Koma anadandaula mwamuna
wake atabwerako chimanjamanja. Mawuwa amanenedwa zinthu
zimene umayembekezera zikakhala kuti sizinachitike, ndiye
ukudandaula kuti bola ukanachita zinthu zina.
Ndikhale nawo analanda malo.
-Si bwino kumangolola anthu osadziwika bwino kuti mukhale
nawo pamudzi kapena kuwapatsa udindo chifukwa pamapeto
pake amakhala eni mudzi. Tizisamala ndi anthu omwe sitiku-
wadziwa bwino.
Ndikudula tsitsi ndi mano.
-Mawuwa munthu amawanena akakhala kuti wavutika kapena
wasauka kwambiri.
Ndim’khulupirira adam’gonetsa m’nkhufi.
-Munthu amene umamudalira, nthawi zina ndi amene amaku-
khumudwitsa kwambiri.
Ndimveke ndine adaphetsa fisi.
-Kususukira kutchuka kumabweretsa tsoka.
Ndinatha Ngombo ndi Akamundi, kuli Achanga ndisanafike.
-Munthu amanena mawuwa podandaula kuti akanadziwa kuti
zabwino zili kutsogolo akanadikira. Amakhala kuti anafulumira
179