Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 178

Miyambi ya Patsokwe chifukwa choti anthu sanamumvetse bwino. Ndabwerera pakamwa pa Mkango. -Mawuwa amenena za munthu amene wapulumuka pamavuto aakulu. Ndagunda, dziko lonse landimva. -Mawuwa amanena za munthu amene watchuka padziko lonse chifukwa cha ntchito zake. Ndakutama kukongola kwako, nzeru zako sindizitama. -Mawuwa amatanthauza kuti, ngakhale munthuyo ali wokongo- la koma ndi wamakhalidwe oipa. Ndakwatiwa kumbuyo, kumaso kulira ena. -Mawuwa amanena za munthu amene wakwatiwa ndi munthu wolemera koma mwamuna wake ndi gojo, sangathe kumupatsa ana. Ndakwatiwa n’kumbuyo komwe. -Wakwatiwa ndi munthu wabwino, wachuma komanso wakha- lidwe labwino. Ndalama zidaphetsa Yesu. -Anthu ena amachita zolakwa zikuluzikulu chifukwa chokonda ndalama. Ndalama zikamayankhula, chilungamo chimakhala chete. -Nthawi zambiri anthu ena amatha kupereka ziphuphu kuti mlandu wawo uyende bwino. Zimenezi zimachititsa kuti osala- kwa amangidwe kapena chilungamo chisaoneke. Ndalowa m’chala. -Mawuwa amatanthauza kudwaladwala. Anganenenso za mun- thu yemwe anali wachuma koma anasauka, moti akusowa pog- wira. 177