Miyambi ya Patsokwe
Mwezi satungira mkanda.
-Ntchito iliyonse ili ndi nthawi yake yoyenera kugwiridwa. Ku-
chita chinthu pa nthawi yolakwika sikuthandiza. Mwachitsanzo,
kufuna kulowetsa ulusi pabowo la singano usiku pa kuwala kwa
mwezi.
Mwezi sayanikira ufa.
-Pali zinthu zina zomwe zimachitika masana okha kapena pa
nthawi yake osati nthawi iliyonse.
Mwezi uli kumwamba, mitengo ili pansi.
-Pali zinthu zina zomwe zili kutali zomwe n’zobisika kwa anthu
koma zina n’zodziwika kwa aliyense ngati mitengo yomwe ili
pansi pano.
Mwini phala sada chala.
-Nthawi zambiri munthu saona kulakwa kwake kapena kwa ana
ake.
Mwiniwake wapha pa mbewu yake.
-Mawuma amanena za munthu yemwe amapha anthu a pabanja
pake kuti achitire zizimba. Zimenezi ndi zina mwa zimene an-
thu a ku Africa kuno amakhulupirira zomwe zilibe umboni kuti
zimathandizadi.
Myang’ana dzuwa adasochera.
-Munthu amene safunsa nthawi zambiri amakumana ndi
mavuto ngati mmene zimakhalira ndi munthu amene amayan-
g’ana kumene kuli dzuwa akamayenda ulendo. Dzuwalo li-
masuntha ndiye amasokonekera n’kusochera.
Myendera mwana salema.
-Munthu akakhala ndi mwana wake satopa kumuyendera.
Tikamachita chinthu sitiyenera kutopa mpaka titachikwaniritsa.
175