Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 175
Miyambi ya Patsokwe
Mwayi ndi mwayi.
-Ngati munthu wapeza mwayi wochita zinazake ndi mwayi
wake basi.
Mwayi sudziwika.
-Tizingochita zomwe tikuganiza kuti zingatithandize.
Mwayi sufanana.
-Anthufe timapeza zinthu mosiyana.
Mwayi sulingana.
-Anthufe timapeza zinthu mosiyana.
Mwayi wa mnzako sagonera pabwalo.
-Si bwino kungochita zinthu chifukwa choti waona kuti wina
zamuyendera bwino. Mwachitsanzo, chifukwa choti wina
wachita chinachake n’kuyenda bwino, si ndiye kuti iwe ukachi-
tanso zomwezo zikuthera bwino.
Mwayi wa munthu mmodzi sangagonere wina pabwalo.
-Mwayi umasiyana. Tisamachite zinthu chifukwa choti anzathu
atachita zomwezo zinawayenera bwino.
Mwayi wamzama wofukula ndi manja.
-Mwayi waukulu kwambiri.
Mwazi ukutuluka pampini.
-Mawu otanthauza kuti pakuchitika zodabwitsa.
Mwendo wa amfumu kulemera.
-Anduna akampempha anthu kuti atumidwa ndi amfumu kuti
apemphe thandizo lawo anthuwo n’kukana ndunazo zimamva
mwendo wa mfumu kulemera. M’mawu ena zimaona kuti
udindo wawowo ndi wolemera kwambiri.
Mweranitu, ukadza kuno subwerera, ndigubula.
-Mwayi kapena nthawi ikapezeka, ndi bwino kuchitiratu chifu-
kwa zamawa sizidziwika.
174