Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 174
Miyambi ya Patsokwe
zinthu zambiri zomwe zingachititse kuti azipitapita ku-
chimbudzi.
Mwana yemwe amasamba m’manja amadya ndi akuluakulu.
-Munthu amene ali ndi khalidwe labwino kapena wolimbikira
ntchito amakondedwa ndi ena ndipo zinthu zimamuyendera
bwino.
Mwandimangitsa madzi m’masamba.
-N’zosatheka kumanga madzi m’masamba. Choncho mawuwa
amatanthauza kuti mwandipusitsa.
Mwandimangitsa madzi m’mayani.
-N’zosatheka kumanga madzi m’masamba. Choncho mawuwa
amatanthauza kuti mwandipusitsa.
Mwandiyesa “kankhuku kadza ndi yani?”
-Mawu otanthauza kuti mukuyesa ndine mlendo?
Mwandiyesa kankhuku kachilendo.
-Mawu otanthauza kuti mukuyesa ndine mlendo?
Mwaupaka matope, mpanje wakanika kulira.
-Ng’oma ikakhala ndi matope siimveka bwino. Tizionetsetsa
kuti zonse zili bwino tisanayambe kuchita zinthu.
Mwauza Kambuku kugwira pakhosi.
-Ngati Kambuku wagwira nyama pakhosi ndi kuti yapita imen-
eyo. Chimodzimodzinso kulekerera anthu kuchita khalidwe
loipa kumakhala ngati kulimbikitsa khalidwelo.
Mwavomera chamutu, mtima wakana.
-Mawu otanthauza kuti simunavomere ndi mtima wonse.
Mwayi kusiyana.
-Anthufe timapeza zinthu mosiyana.
173