Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 173
Miyambi ya Patsokwe
a Ng’azi.
Mwana wa Ng’ona sakulira dziwe limodzi.
-Mwamuna sakulira malo amodzi. Amafunika kuyendayenda
kuti akasake ndalama zothandizira mkazi komanso abale ake.
Mwana wa Ng’ona salephera kuyangalala.
-Nthawi zambiri ana amatengera luso la makolo awo. Ng’ona
imayendayenda m’madzi chifukwa ndi zimene makolo awo
amachita.
Mwanapiye kunyera m’nyumba awonera mayi ake.
-Zimene makolo amachita ndi zimene ana amatengera.
Mwana wa Nkhuku chenjera, Kabawi watulukira.
-Mawuwa amakonda kunena ndi ogwira ntchito akamachenjeza
anzawo kuti abwana kapena owayang’anira akubwera.
Mwana wa pang’oma salephera kuyangala.
-Nthawi zambiri mwana amatengera khalidwe la makolo ake.
Mwana waulemu amakodza kwambiri.
-Munthu waulemu amapeza zinthu zambiri pakati pa anzake.
M’mawu ena amadya zambiri zomwe zimachititsa kuti az-
ingokodzakodza.
Mwana wokhulupirika amakodza pogona.
-Mwambiwu amaunena akamalimbikitsa mwana kapena mun-
thu wina kuti akakhala wotumika kapena wokhulupirika anthu
azimupatsa zinthu zambiri zomwe zingachititse kuti azikodza
pogona chifukwa chokhuta.
Mwana wokhulupirika amanyera nchimba waukulu.
-Mwambiwu ndi woumitsa pakamwa, koma ena amaunena
momasuka akamalimbikitsa mwana kapena munthu wina kuti
akakhala wotumika kapena wokhulupirika anthu azimupatsa
172