Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 172

Miyambi ya Patsokwe Mwana wa mnzako ndiye ‘kasambe m’manja,’ wako ndiye ‘tazingodya!’ -Tisamachitire nkhanza ana a anzathu. Tiziwachitira mofanana ndi ana athu. Mwana wa munthu wopatsa sagona ndi njala. -Munthu ukamakhala bwino ndi anthu, ukamawathandiza ndi kuwachitira zabwino, ngakhale umwalire ana ako samadza- zunzika. Amadzawathandiza pokumbukira khalidwe lako labwino. Mwana wa mwini ndi gaga, saundika. -N’zovuta kuthandiza mwana wa mwini kusintha khalidwe. Ukamupatsa chilango amaona ngati nkhanza. Ena ngakhale akadzakula amatha kudzakuthawa n’kupita kwa abale awo. Mwana wa mwini ndi tsabola wokomera m’kamwa, akagwa m’maso ndi nkhondo. -Ana a anthu ena akhoza kungooneka abwino pamaso, koma nthawi zina akhoza kuyambitsa chipwirikiti komanso kuwonon- ga zinthu zathu. Mwana wa Ng’ombe amadya udzu, anaonekera amake kudya udzu. -Ana amatengera makolo awo pa zabwino kapena zoipa. Mwana wa Ng’ona alibe makutu, kumva kwake ndi kum’pan- da. -Ngati mwana samvera makolo, nthawi zina ndi bwino kumu- langa mwina pomukwapula kapena kumupatsa chilango china. Mwana wa Ng’ona ndi uyo ali pamchira, wa pambuyo ngwa Ng’azi. -Ngakhale ana amafanana ndi makolo awo, ngati samamvera malangizo awo amadzakumana ndi mavuto, amakhala ngati ana 171