Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 171

Miyambi ya Patsokwe kwambiri kapena ndi mtsogoleri wa dziko. Mwana sasowa amake. -Ana kapena ziweto zimadziwa makolo komanso mbuye wawo. Munthu sulephera kuzindikira chinthu chako. Mwana ukam’zoloweza kukwera pathandala, saleka. -Mwana amachita zimene makolo ake amuphunzitsa. Aka- muphunzitsa zabwino, mwanayo amakhalanso wabwino. Mwana wa “kaya” sachira. -Munthu wina akamadwala si bwino kunena zokhumudwitsa, koma kumulimbikitsa ngakhale ukudziwiratu kuti sachira. Ena akatifunsa zinazake tiyenera kunena motsindika osati kumaka- yikira. Mwana wa a Matumbo wamwalira, adzanena ndi a M’masom- wada. -Mkuluwikowu umanena zoti munthu ali ndi njala. Mwana wa amfumu anaotha uta wake. -Chifukwa chodalira udindo wa bambo ake, mwana wa amfumu anaotcha uta wake modzionetsera. Si bwino kunyada kapena kudzionetsera chifukwa zimenezi zikhoza kutayitsa munthu zinthu zambiri ngati chuma. Mwana wa mfulu ndi mbatata, ukaongola wathyola. -Nthawi zambiri anthu omwe ndi otchuka kapena audindo waukulu amavuta kuwalangiza. Ukalimbana nawo umakumana ndi mavuto ndi iweyo. Mwana wa mnzako ndi wako yemwe, ukachenjera manja udzadya naye. -Tizikonda ana a anzathu monga ana anthu chifukwa tsiku lina anawo mwinanso atakula akhoza kudzatithandiza, tikhoza kud- zadya zawo. 170