Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 170
Miyambi ya Patsokwe
Mwana akalilira nyanga ya nsatsi, m’semere im’fotere yekha
kumanja.
-Munthu akamafuna zinthu zopanda pake ndi bwino kumusiya
kuti awone yekha zotsatira zake. Zimenezi zingamuthandize
kuti amvetse chifukwa chake mumamukaniza ndipo sanga-
dzabwerezenso.
Mwana amalira ndi mkodzo wake womwe.
-Anthu achibwana amachita zinthu zomwe pambuyo pake
amadzanong’oneza nazo bondo n’kumafuna kuti ena awathan-
dize.
Mwana amaopa kachirombo kakamuluma.
-Kuti munthu adziwe kuti chinthuchi n’choopsa, amaphunzira
akakumana ndi mavuto.
Mwana amene amasamba m’manja amadya ndi akuluakulu.
-Mwana wakhalidwe amapeza zabwino komanso amakondedwa
ndi akuluakulu.
Mwana m’nyanja alimbikira mpani wake.
-Munthu aliyense amalimbikira kuchita zinthu zake. Amaonet-
setsa kuti zachitika bwino kwambiri koposa mmene akanachitira
za ena. Mawuwa amanenedwanso munthu akamachita zinthu
zokondera pa mlandu wa m’bale wake.
Mwana ndi bango, akafa amaphuka wina.
-Mawuwa amanenedwa potonthoza makolo omwe mwana
wawo wamwalira kuti asadandaule Mulungu adzawapatsa
wina.
Mwana sakulira nakubala.
-Ngakhale mwana ataphunzira bwanji kapena atakula chamtun-
du wanji, ayenera kumalemekezabe makolo ake. Angachite zim-
enezi ngakhale zitakhala kuti aliyense amamulemekeza
169