Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 17

Miyambi ya Patsokwe Apawo ndi mchenga, madzi apita pansi. -Munthu ukakhala mlendo sudziwa zomwe eni mudzi akupan- gana, umangoona zikuchitika. Ali ngati mchenga omwe sudziwika kuti pansi pake pali madzi. Choncho, ukakhala pamudzi umayenera kusamala chifukwa nthawi zina amaoneka ngati sagwirizana pomwe amagwirizana ndithu. Apawo ndi mizu ya kachere, amakumana pansi. -Munthu ukakhala mlendo sudziwa zomwe eni mudzi akupan- gana, umangoona zikuchitika. Ali ngati mizu ya kachere yomwe sudziwika kuti yakumana pansi. Choncho, ukakhala pamudzi umayenera kusamala chifukwa nthawi zina amaoneka ngati sag- wirizana pomwe amagwirizana ndithu. Atadya anamwera. -Chilichonse chimakhala ndi nthawi yake. Atambala awiri salira m’khola limodzi. -N’zovuta kuti anthu awiri azilamulira chinthu chimodzi. Atambwali sametana, amaopa kuchekana. -Nthawi zambiri anthu amene amachita zofanana zimakhala zovuta kuti apusitsane. Atambwali sangapitane pansi. Atambwali sametana, amawopa kuchekana. -Ochenjera okhaokha sangapusitsane. Aulesi sangapate kanthu. -Palibe chinthu cholongosoka chimene munthu waulesi anga- peze. Nthawi zambiri usiwa umamugwira munthu wotereyu ngati kapolo. Awonenji adapha mvuwu m’mono. -Munthu aliyense ali ndi mwayi wake. Choncho, si bwino ku- ganiza kuti anthu ena ooneka onyozeka sangapeze mwayi. 16